Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 22:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Alabori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

13. Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukuru; popeza atate athu sanamvera mau a buku ili, kucita monga mwa zonse zotilemberamo.

14. Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tlkiva, mwana wa Harasi, wosunga zobvala za mfumu; analikukhala iye m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nalankhula naye.

15. Ndipo Hulida ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

16. Atero Yehova, Ta, onani, nditengera maloano coipa, ndi iwo okhalamo, cokwaniritsa mau onse a m'buku adaliwerenga mfumu ya Yuda;

17. popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace mkwiyo wanga udzayakira malo ana wosazimikanso.

18. Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kunena za mau udawamva,

19. popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzicepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ana ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zobvala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.

20. Cifukwa cace, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako coipa conse ndidzacifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 22