Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 22:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.

2. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lace, osapambukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

3. Ndipo kunali caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, ku nyumba ya Yehova, ndi kuti,

4. Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;

5. iwo azipereke kwa ogwira nchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,

6. kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.

7. Koma sanawawerengera ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anacita mokhulupirika.

8. Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.

9. Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m'nyumba, nazipereka m'dzanja la anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 22