Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 20:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo kunali, asanaturukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,

5. Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, nelidzakuciritsa, tsiku lacitatu udzakwera kumka ku nyumba ya Yehova.

6. Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asuri; ndidzacinjiriza mudzi uno, cifukwa ca Ine ndekha, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.

7. Nati Yesaya, Tenga ncinci yankhuyu. Naitenga, naiika papfundo, nacira iye.

8. Nati Hezekiya kwa Yesaya, Cizindikilo cace nciani kuti Yehova adzandiciza, ndi kuti ndidzakwera kumka ku nyumba ya Yehova tsiku lacitatu?

9. Nati Yesaya, Cizindikilo ndici akupatsa Yehova, kuti Yehova adzacicita conena iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?

10. Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.

11. Napfuulirakwa Yehova Yesayamneneriyo, nabweza iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 20