Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 20:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2. Pamenepo anatembenuzira nkhope yace kukhoma, napemphera kwa Yehova, ndi kuti,

3. Mukumbukile Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'coonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kucita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukuru.

4. Ndipo kunali, asanaturukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,

5. Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, nelidzakuciritsa, tsiku lacitatu udzakwera kumka ku nyumba ya Yehova.

6. Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asuri; ndidzacinjiriza mudzi uno, cifukwa ca Ine ndekha, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.

7. Nati Yesaya, Tenga ncinci yankhuyu. Naitenga, naiika papfundo, nacira iye.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 20