Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ace, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.

9. Ndipo kunali caka cacinai ca mfumu Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli Salimanezeri mfumu ya Asuri anakwerera Samariya, naumangira misasa.

10. Pakutha pace pa zaka zitatu anaulanda, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Israyeli analanda Samariya.

11. Ndipo mfumu ya Asuri anacotsa Aisrayeli kumka nao ku Asuri, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi;

12. cifukwa sanamvera mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira cipangano cace, ndico zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvera kapena kuzicita.

13. Caka cakhumi ndi zinai ca Hezekiya Sanakeribu mfumu ya Asuri anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.

14. Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundicokere; cimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.

15. Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba yamfumu.

16. Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golidi wa pa zitseko za Kacisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asuri.

17. Ndipo mfumu ya Asuri anatuma nduna ndi ndoda ndi kazembe ocokera ku Lakisi ndi khamu lalikuru la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima ku mcerenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsaru.

18. Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawaturukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolemba mbiri.

19. Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Cikhulupiriro ici ncotani ucikhulupirira?

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18