Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 17:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Koma sanamvera, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirira Yehova Mulungu wao.

15. Ndipo anakaniza malemba ace, ndi cipangano anacicita ndi makolo ao, ndi mboni zace anawacitira umboni nazo, natsata zopanda pace, nasanduka opanda pace, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asacite monga iwowa.

16. Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, ana a ng'ombe awiri, napanga cifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.

17. Napititsa ana ao amuna ndi akazi kumoto, naombeza ula, nacita zanyanga, nadzigulitsa kucita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.

18. Cifukwa cace Yehova anakwiya naye Israyeli kwakukuru, nawacotsa pamaso pace osatsala mmodzi, koma pfuko la Yudalokha.

19. Yudansosanasunga malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israyeli amene adawaika.

20. Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israyeli, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pace.

21. Pakuti anang'amba Israyeli, kumcotsa ku nyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati; Yerobiamu naingitsa Israyeli asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukuru.

22. Nayenda ana a Israyeli m'zolakwa zonse za Yerobiamu, zimene anazicita osazileka;

23. mpaka Yehova adacotsa Israyeli pamaso pace, monga adanena mwa dzanja la atumiki ace onse aneneriwo. Momwemo Israyeli anacotsedwa m'dziko lao kumka nao ku Asuri mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 17