Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 15:29-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Masiku a Peka mfumu ya Israyeli anadza Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, nalanda Ijoni, ndi Abeli-BeteMaaka, ndi Yanoa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Gileadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafitali; nawatenga andende kumka nao ku Asuri.

30. Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamcitira ciwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwace caka ca makumi awiri ca Yotamu mwana wa Uziya.

31. Macitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

32. Caka caciwiri ca Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israyeli, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

33. Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu: zisanu polowa ufumu wace, nakhalamfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndipo dzina la mace ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

34. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anacita monga mwa zonse anazicita atate; wace Uziya.

35. Komatu sanaicotsa misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga cipata ca kumtunda ca nyumba ya Yehova.

36. Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazicita, sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

37. Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye.

38. Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ace, namuika pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; nakhala mfumu m'malo mwace Ahazi mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 15