Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 15:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israyeli ndaramazi, nasonkhetsa acuma, yense masekeli makumi asanu a siliva: kuti azipereke kwa mfumu ya Asuri. Nabwerera mfumu ya Asuri osakhala m'dzikomo.

21. Macitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazicita, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

22. Nagona Menahemu ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Pekahiya mwana wace.

23. Caka ca makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.

24. Nacita coipa pamaso pa Yehova, sanaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

25. Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wace, anamcitira ciwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobo ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya ku nyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Gileadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwace.

26. Macitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazicita, taonani zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

27. Caka ca makumi asanu mphambu ziwiri ca Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.

28. Nacita coipa pamaso pa Yehova: osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli,

29. Masiku a Peka mfumu ya Israyeli anadza Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, nalanda Ijoni, ndi Abeli-BeteMaaka, ndi Yanoa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Gileadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafitali; nawatenga andende kumka nao ku Asuri.

30. Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamcitira ciwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwace caka ca makumi awiri ca Yotamu mwana wa Uziya.

31. Macitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 15