Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 14:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Natenga golidi ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca m'nyumba ya mfumu, acikole omwe; nabwera kumka ku Samariya,

15. Macitidwe ena tsono a Yoasi adazicita, ndi mphamvu yace, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

16. Nagona Yoasi ndi makolo ace, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Yerobiamu mwana wace.

17. Ndipo Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yoasi mwana wa Yoahazi mfumu ya Israyeli, zaka khumi ndi zisanu.

18. Macitidwe ena tsono a Amaziya, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

19. Ndipo anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.

20. Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 14