Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 14:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka caciwiri ca Yoasi mwana wa Yoahazi mfumu ya Israyeli, Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

2. Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; dzina la mace ndiye Yoadana wa ku Yerusalemu.

3. Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lace; nacita monga mwa zonse anazicita Yoasi atate wace.

4. Koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5. Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m'dzanja lace, anakantha anyamata ace amene adakantha mfumu atate wace;

6. koma ana a ambandawo sanawapha, monga mwalembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulak wa kwa iye yekha.

7. Anapha Aedomu m'Cigwa ca Mcere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, naucha dzina lace Yokiteli mpaka lero lino.

8. Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yoasi mwana wa Yoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani tionane maso.

9. Natumiza Yoasi mfumu ya Israyeli kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; ndipo Inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebano, nipondereza mtungwiwo.

10. Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;

11. Koma Amaziya sanamvera. Motero anakwera Yoasi mfumu ya Israyeli, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betisemesi, ndiwo wa Yuda.

12. Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israyeli, nathawira yense kuhema kwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 14