Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 13:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Nati iye, Tengani mibvi; naitenga, Nati kwa mfumu ya Israyeli, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

19. Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.

20. Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amoabu analowa m'dziko poyambira caka.

21. Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima ciriri.

22. Ndipo Hazaeli mfumu ya Aramu anapsinja Israyeli masiku onse a Yoahazi.

23. Koma Yehova analeza nao mtima, nawacitira cifundo, nawatembenukira; cifukwa ca cipangano cace ndi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 13