Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 13:16-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Nati kwa mfumu ya Israyeli, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ace pa manja a mfumu.

17. Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Mubvi wa cipulumutso wa Yehova ndiwo mubvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha.

18. Nati iye, Tengani mibvi; naitenga, Nati kwa mfumu ya Israyeli, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

19. Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.

20. Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amoabu analowa m'dziko poyambira caka.

21. Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima ciriri.

22. Ndipo Hazaeli mfumu ya Aramu anapsinja Israyeli masiku onse a Yoahazi.

23. Koma Yehova analeza nao mtima, nawacitira cifundo, nawatembenukira; cifukwa ca cipangano cace ndi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pace.

24. Nafa Hazaeli mfumu ya Aramu, nakhala mfumu m'malo mwace Benihadadi mwana wace.

25. Ndi Yoasi mwana wa Yoahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wace ndi nkhondo. Yoasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 13