Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 12:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Yoasi anati kwa ansembe, Landirani ndarama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo ndarama za otha msinkhu, ndarama za munthu ali yense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwace kuti abwere nazo ku nyumba ya Yehova.

5. Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, pali ponse akapeza pogamuka.

6. Koma kunali, caka ca makumi awiri mphambu zitatu ca Yoasi sanathe kukonza mogamuka nyumba.

7. Pamenepo mfumu Yoasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndarama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.

8. Nabvomera ansembe kusalandiranso ndarama za anthu, kapena kukonza mogamuka nvumba.

9. Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola ciboo pa cibvundikilo cace, naliika pafupi pa guwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndarama zonse anabwera nazo anthu ku nyumba ya Yehova,

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 12