Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 12:18-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma Yoasi mfumu ya Yuda: anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yoramu, ndi Ahaziya, makolo ace, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zace zace, ndi golidi yense anampeza pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Aramu; motero anabwerera kucoka ku Yerusalemu.

19. Macitidwe ena tsono a Yoasi ndi zonse adazicita sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

20. Ndipo anyamata ace ananyamuka, napangana, nakantha Yoasi ku nyumba ya Milo potsikira ku Silo.

21. Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yosabadi mwana wa Someri, anyamata ace, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ace m'mudzi wa Davide; ndi Amaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 12