Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 10:33-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. kuyambira ku Yordano kum'mawa, dziko lonse la Gileadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroeri, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Gileadi ndi Basana.

34. Ndipo macitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace yonse, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafwnu a Israyeli

35. Nagona Yehu ndi makolo ace, namuika m'Samariya. Ndi Yehoahazi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

36. Ndipo masiku ace akukhala Yehu mfumu ya Israyeli m'Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 10