Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 6:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo mucitire ulemu Mulungu wa lsrayeli; kuti kapena adzaleza dzanja lace pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.

6. Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aaigupto ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sana lola anthuwo amuke, iye atacita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?

7. Cifukwa cace tsono, tengani, nimukonze gareta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli cikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagareta, muzicotsere ana ao kunka nao kwanu;

8. ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaretapo; nimuike zokometsera zagolidi, zimene muzipereka kwa iye ngati nsembe yoparamula, m'bokosi pam bali pace; nimulitumize licoke.

9. Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire ace ace ku Betisemesi, iye anaticitira coipa ici cacikuru; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, siliri lace; langotigwera tsokali.

10. Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagareta, natsekera anao kwao;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 6