Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 30:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakuru, ana amuna kapena ana akazi, kapena cuma kapena dna ciri conse ca zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse.

20. Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipitikitsa patsogolo pa zoweta zao zao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide.

21. Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anaturuka kucingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.

22. Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pace a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wace ndi ana ace, kuti acoke nao namuke.

23. Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.

24. Ndipo ndani adzabvomerezana nanu mrandu uwu? Pakuti monga gawo lace la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lace la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana cimodzimodzi.

25. Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ici, cikhale lemba ndi ciweruzo pa Aisrayeli.

26. Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilaga, anatumizako za zofunkhazo kwa akuru a Yuda, ndiwo abwenzi ace, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 30