Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 30:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. nampatsanso cigamphu ca ncinci ya nkhuyu ndi ncinci ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wace unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya cakudya, osamwa madzi.

13. Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? ufumira kuti? Nati iye, Ndiri mnyamata wa ku Aigupto, kapolo wa M-amaleki; mbuye wanga anandisiya, cifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.

14. Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebi; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilaga ndi moto.

15. Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.

16. Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, cifukwa ca cofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.

17. Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wace; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamila, nathawa.

18. Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleki, napulumutsa akazi ace awiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 30