Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 30:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ace ku Zikilaga tsiku lacitatu, Aamaleki adaponya nkhondo yobvumbulukira kumwera, ndi ku Zikilaga, nathyola Zikilaga nautentha ndi moto;

2. nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akuru ndi ang'ono; sanapha mmodzi, koma anawatenga, namuka.

3. Ndipo pamene Davide ndi anthu ace anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao amuna ndi akazi anatengedwa ukapolo.

4. Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.

5. Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinoamu wa ku Jezreeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.

6. Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi cisoni, yense cifukwa ca ana ace amuna ndi akazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wace.

7. Ndipo Davide ananena ndi Abyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.

8. Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Lonriola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.

9. Comweco Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.

10. Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, cifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.

11. Ndipo ena anapeza M-aigupto kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa cakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;

12. nampatsanso cigamphu ca ncinci ya nkhuyu ndi ncinci ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wace unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya cakudya, osamwa madzi.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 30