Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 29:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kuturuka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona coipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.

7. Cifukwa cace, bwerera, numuke mumtendere, kuti angaipidwe mtima nawe akalonga a Afilisti.

8. Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinacitanji? Ndipo munapeza ciani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndiri pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?

9. Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, iye asamuke nafe kunkhondoko.

10. Cifukwa cace ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutaca.

11. Comweco Davide analawirira, iye ndi anthu ace, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera ku Jezreeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 29