Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 29:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani?

6. Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kuturuka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona coipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.

7. Cifukwa cace, bwerera, numuke mumtendere, kuti angaipidwe mtima nawe akalonga a Afilisti.

8. Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinacitanji? Ndipo munapeza ciani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndiri pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?

9. Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, iye asamuke nafe kunkhondoko.

10. Cifukwa cace ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutaca.

11. Comweco Davide analawirira, iye ndi anthu ace, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera ku Jezreeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 29