Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 29:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisrayeli anamanga ku citsime ca m'Jezreeli.

2. Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ace ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.

3. Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa acitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Sauli, mfumu ya Israyeli, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.

4. Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwace kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yace? Si ndi mitu ya anthu awa?

5. Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani?

6. Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kuturuka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona coipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 29