Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 23:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsono anauza Davide, kuti, Onani Afilisti alikuponyana ndi Keila, nafunkha za m'madwale.

2. Cifukwa cace Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.

3. Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m'mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti.

4. Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.

5. Comweco Davide ndi anthu ace anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.

6. Ndipo kunali kuti Abyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lace.

7. Ndipo anthu anauza Sauli kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Sauli anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 23