Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 22:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Motero Davide anacoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ace ndi banja lonse la atate wace anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.

2. Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.

3. Ndipo Davide anacoka kumeneko kunka ku Mizipa wa ku Moabu; nati kwa mfumu ya Moabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga aturuke nakhale nanu, kufikira ndidziwa cimene Mulungu adzandidtira.

4. Ndipo anawatenga kumka nao pamaso pa mfumu ya Moabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo.

5. Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; cokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anacokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.

6. Pakumva Sauli kuti anadziwika Davide, ndi anthu ace akukhala naye, Sauti analikukhala m'Gibeya, patsinde pa mtengo wa kumsanje, m'dzanja lace munali mkondo wace, ndi anyamata ace onse anaimirira pali iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 22