Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 21:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anafika ku Nobi kwa! Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?

2. Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira nchito, ninena nane, Asadziwe munthu ali yense kanthu za nchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.

3. Cifukwa cace tsono muli ndi ciani? mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena ciri conse muli naco.

4. Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndiribe mkate wacabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.

5. Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; cicokere ine, zotengera za anayamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wacabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?

6. Comweco wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adaucotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anacotsa winawo.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 21