Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 20:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo undionetsere cifundo ca Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;

15. komanso usaleke kucitira cifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse; mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Da vide pa dziko lapansi.

16. Comweco Jonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.

17. Ndipo Jonatani anamlumbiritsa Davide kaciwiri, cifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.

18. Tsono Jonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.

19. Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mrandu uja, nukhale pa mwala wa Ezeri.

20. Ndipo ine ndidzaponya mibvi itatu pambali pace, monga ngati ndirikuponya pacandamali.

21. Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune mibviyo, Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mibvi iri cakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.

22. Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mibvi iri kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.

23. Ndipo za cija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 20