13. Mulungu alange Jonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukucitira coipa, ine osakuululira, ndi kukucotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.
14. Ndipo undionetsere cifundo ca Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;
15. komanso usaleke kucitira cifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse; mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Da vide pa dziko lapansi.
16. Comweco Jonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.
17. Ndipo Jonatani anamlumbiritsa Davide kaciwiri, cifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.