Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 20:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Jonatani, Ndacitanji ine? kuipa kwanga kuli kotani? ndi chimo langa la pamaso pa atate wanu ndi ciani, kuti amafuna moyo wanga?

2. Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate, wanga sacita kanthu kakakuru kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji cinthu cimeneci? Si kutero ai.

3. Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Jonatani asadziwe ici, kuti angamve cisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazilimodzi.

4. Ndipo Jonatani anati kwa Davide, Ciri conse mtima wako unena, ndidzakucitira.

5. Nati Davide kwa Jonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lacitatu madzulo ace.

6. Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pacaka ya banja lao lonse.

7. Tsono akati, Cabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundicitira coipa.

8. Cifukwa cace ucitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamcititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli coipa ciri conse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 20