Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 2:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Hana anapemphera, natiMtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova,Nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova;Pakamwa panga pakula kwa adani anga;Popeza ndikondwera m'cipulumutsocanu.

2. Palibe wina woyera ngati Yehova;Palibe wina koma Inu nokha;Palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

3. Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero;M'kamwa mwanu musaturuke zolulutsa;Cifukwa Yehova ali Mulungu wanzeru,Ndipo iye ayesa zocita anthu.

4. Mauta a amphamvu anathyoka,Koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'cuuno.

5. Amene anakhuta anakasuma cakudya;Koma anjalawo anacira;Inde cumba cabala asanu ndi awiri:Ndipo iye amene ali ndi ana ambiri acita liwondewonde.

6. Yehova amapha, napatsa moyo:Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.

7. Yehova asaukitsa, nalemeza;Acepetsa, nakuzanso.

8. Amuutsa waumphawi m'pfumbi,Nanyamula wosowa padzala,Kukamkhalitsa kwa akalonga;Ndi kuti akhale naco colowa ca cimpando ca ulemerero;Cifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova,Ndipo iye anakhazika dziko pa izo,

9. Adzasunga mapazi a okoodedwaace,Koma oipawo adzawakhalitsa cete mumdima;Pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu,

10. Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika;Kumwamba iye adzagunda pa iwo:Yehova adzaweruza malekezero a dziko:Ndipo adzapatsa mphamvu mfumuyace,Nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wace.

11. Ndipo Elikana anauka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo.

12. Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 2