Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 19:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Sauli analankhula kwa Jonatani mwana wace, ndi anyamata ace onse kuti amuphe Davide.

2. Koma Jonatani mwana wa Sauli anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Jonatani anauza Davide, nati, Sauli atate wanga alikufuna kukupha; cifukwa cace tsono ucenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale;

3. ndipo ine ndidzaturuka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.

4. Ndipo Jonatani analankhula ndi atate wace mobvomereza Davide, nanena naye, Mfumu asacimwire mnyamata wace Davide; cifukwa iyeyo sanacimwira inu, ndipo nchito zace anakucitirani zinali zabwino ndithu;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 19