Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 16:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

8. Pamenepo Jese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samueli. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankha.

9. Pamenepo Jese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankha.

10. Ndipo Jese anapititsapo ana ace amuna asanu ndi awiri. Koma Samueli anati kwa Jese, Yehova sanawasankha awa.

11. Ndipo Samueli anati kwa Jese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samueli anati kwa Jese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.

12. Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 16