Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 16:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Samueli anacita cimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akuru a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?

5. Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Jese ndi ana ace, nawaitanira kunsembeko.

6. Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pace.

7. Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

8. Pamenepo Jese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samueli. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankha.

9. Pamenepo Jese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankha.

10. Ndipo Jese anapititsapo ana ace amuna asanu ndi awiri. Koma Samueli anati kwa Jese, Yehova sanawasankha awa.

11. Ndipo Samueli anati kwa Jese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samueli anati kwa Jese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.

12. Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.

13. Pamenepo Samueli anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ace; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samueli ananyamuka, Danks ku Rama.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 16