Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 16:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pamenepo Samueli anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ace; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samueli ananyamuka, Danks ku Rama.

14. Koma mzimu wa Yehova unamcokera Sauli, ndi mzimu woipa wocokera kwa Yehova unambvuta iye.

15. Ndipo anyamata a Sauli ananena naye, Onani tsopano, mzimu woipa wocokera kwa Mulungu ulikubvuta inu.

16. Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuyimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wocokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzayimba ndi dzanja lace, ndipo mudzakhala wolama.

17. Ndipo Sauli anati kwa anyamata ace, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuyimba bwino, nimubwere naye kwa ine.

18. Ndipo mnyamata wace wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Jese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuyimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wocenjera manenedwe ace; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.

19. Cifukwa cace Sauli anatumiza mithenga kwa Jese, nati, Vnditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.

20. Ndipo Jese anatenga buru namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi: mwana wa mbuzi, nazitumiza kwa Sauli ndi Davide mwana wace.

21. Ndipo Davide anafika kwa Sauli, naima pamaso pace; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zace.

22. Ndipo Sauli anatumiza kwa Jese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima.

23. Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wocokera kwa Mulungu unali pa Sauli, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lace; comweco Sauli anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamcokeraiye.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 16