Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 15:33-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo Samueli anati, Monga lupanga lako linacititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samueli anamdula Agagi nthuli nthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.

34. Pamenepo Samueli ananka ku Rama; ndi Sauli anakwera kunka ku nyumba yace ku Gibeya wa Sauli.

35. Ndipo Samueli sanadzanso kudzaona Sauli kufikira tsiku la imfa yace; koma Samueli analira cifukwa ca Sauli; ndipo Yehova anali ndi cisoni kuti anamlonga Sauli mfumu ya Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 15