Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 15:31-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Comweco Samueli anabwerera natsata Sauli; ndi Sauli analambira Yehova.

32. Ndipo Samueli anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleki. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

33. Ndipo Samueli anati, Monga lupanga lako linacititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samueli anamdula Agagi nthuli nthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.

34. Pamenepo Samueli ananka ku Rama; ndi Sauli anakwera kunka ku nyumba yace ku Gibeya wa Sauli.

35. Ndipo Samueli sanadzanso kudzaona Sauli kufikira tsiku la imfa yace; koma Samueli analira cifukwa ca Sauli; ndipo Yehova anali ndi cisoni kuti anamlonga Sauli mfumu ya Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 15