Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 13:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala cikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pace; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ace, cifukwa inu simunasunga cimene Yehova anakulamulirani.

15. Ndipo Samueli anauka nacoka ku Giligala kunka ku Gibeya wa ku Benjamini. Ndipo Sauli anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.

16. Ndipo Sauli, ndi Jonatani mwana wace, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.

17. Ndipo owawanya anaturuka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofra, ku dera la Sauli;

18. gulu lina linalowa njira yonka ku Betihoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku cigwa ca Zeboimu kucipululuko.

19. Ndipo m'dziko lonse la Israyeli simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisrayeli angadzisulire malupanga kapena mikondo;

20. koma Aisrayeli onse adafotsikira kwa Afilisti, kuti awasaniire munthu yense cikhasu cace, colimira cace, nkhwangwa yace, ndi khasu lace;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 13