19. Ndipo anthu onse ananena ndi Samueli, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza coipa ici, cakuti tinadzipemphera mfumu.
20. Ndipo Samueli ananena kwa anthuwo, Musaope; munacitadi coipa ici conse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;
21. musapambukire inu kutsata zinthu zacabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza ziri zopanda pace.
22. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace cifukwa ca dzina lace lalikuru; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a iye yekha.
23. Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kucimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.
24. Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuruzo iye anakucitirani.
25. Koma mukaumirirabe kucita coipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe.