Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 11:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo m'mawa mwace Sauli anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo m'ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.

12. Ndipo anthu anati kwa Samueli, Ndani iye amene anati, Kodi Sauli adzatiweruza ife? tengani anthuwo kuti tiwaphe.

13. Koma Sauli anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anacita cipulumutso m'lsrayeli.

14. Ndipo Samueli ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.

15. Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Sauli mfumu pamaso pa Yehova m'Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Sauli ndi anthu onse a Israyeli anakondwera kwakukuru.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 11