Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 10:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. nanena ndi ana a Israyeli, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli kuti, Ine ndinaturutsa Israyeli m'Aigupto, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aaigupto, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani;

19. koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Cifukwa cace tsono mudzionetse pamaso pa Mulungu mafuko mafuko, ndi magulu magulu.

20. Comweco Samueli anayandikizitsa mafuko onse a Israyeli, ndipo pfuko la Benjamini linasankhidwa.

21. Nayandikizitsa pfuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Sauli mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.

22. Cifukwa cace anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.

23. Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'cifuwa.

24. Ndipo Samueli ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anapfuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.

25. Pamenepo Samueli anafotokozera anthu macitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samueli anauza anthu onse amuke, yense ku nyumba yace,

26. Ndi Sauli yemwe anamuka ku nyumba yace ku Gibeya; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.

27. Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala cete.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 10