Ndipo Samueli ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anapfuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.