Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 22:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Cokhaci, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israyeli, kuti usunge cilamulo ca Yehova Mulungu wako,

13. Momwemo udzalemerera, ukasamalira kucita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israyeli; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.

14. Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwi zikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, osayesa kulemera kwace, pakuti zidacurukaeli; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.

15. Uli naonso anchito ocuruka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akucita nchito ziri zonse;

16. golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nucite, Yehova akhale nawe.

17. Davide analangizanso akalonga a Israyeli athanelize Solomo mwana wace, ndi kuti,

18. Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? sanakupumulitsani pambali ponse? pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ace.

19. Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la cipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, ku nyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 22