Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 12:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. wacisanu ndi cimodzi Atai, wacisanu ndi ciwiri Elieli,

12. wacisanu ndi citatu Yohanani, wacisanu ndi cinai Elzabadi,

13. wakhumi Yeremiya, wakhumi ndi cimodzi Makibanai.

14. Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkuru wa iwo anayang'anira cikwi cimodzi.

15. Awa ndi omwe aja anaoloka Yordano mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ace onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.

16. Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide.

17. Ndipo Davide anaturuka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe ciwawa, Mulungu wa makolo athu acione ndi kucilanga.

18. Pamenepo mzimu unabvala Amasai, ndiye wamkuru wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tibvomerezana nanu mwana wa Jese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akuru a magulu.

19. Ena a Manase omwe anapambukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Sauli, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atacita upo, anamuuza acoke, ndi kuti, Adzapambukira kwa mbuye wace Sauli ndi kutisandulikira.

20. Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 12