Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Davide atate wanga anafuna m'mtima mwace kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

18. Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m'mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unacita bwino kuti m'mtima mwako unatero.

19. Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzaturuka m'cuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.

20. Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ace analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wacifumu wa Israyeli monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

21. Ndipo ndakonzera malo likasalo, m'mene muli cipangano ca Yehova, cimene anapangana ndi makolo athu pamene anawaturutsa m'dziko la Aigupto.

22. Ndipo Solomo anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israyeli, natambasulira manja ace kumwamba, nati,

23. Yehova Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu wolingana ndi inu m'thambo la kumwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira cipangano ndi cifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8