Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo kunacitika ataturuka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova,

11. ndipo ansembe sanakhoza kuimirira kurumikira cifukwa ca mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzazanyumba ya Yehova.

12. Pamenepo Solomo anati, Yehova ananena kuti adzakhala m'mdima waukuru.

13. Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo inu nthawi zosatha.

14. Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yace, nidalitsa msonkhano wonse wa Israyeli, Ndi msonkhano wonse wa Israyeli unaimirira.

15. Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israyeli amene analankhula m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lace, nati,

16. Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga Aisrayeli m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse mwa mafuko onse a Israyeli kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisrayeli.

17. Ndipo Davide atate wanga anafuna m'mtima mwace kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

18. Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m'mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unacita bwino kuti m'mtima mwako unatero.

19. Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzaturuka m'cuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.

20. Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ace analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wacifumu wa Israyeli monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8