Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:47-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Ndipo Solomo anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinacuruka ndithu; kulemera kwace kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.

48. Ndipo Solomo anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Mulungu: guwa la nsembe lagolidi, ndi gome lagolidi loikapo mikate yoonekera;

49. ndi zoikapo nyali za golidi woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, cakuno ca monenera, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolidi;

50. ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira mota za golidi woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolidi, za zitseko za cipinda ca m'katimo, malo opatulikitsa, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kacisi.

51. Motero nchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomo anacitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo analonga zinthu adazipatula Davide atate wace, ndizo siliva ndi golidi ndi zipangizo zomwe naziika mosungira cuma ca nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7