Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:40-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga nchito yonse anaicitira mfumu Solomo ya m'nyumba ya Yehova.

41. Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo,

42. ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,

43. ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi ziri pa maphakawo,

44. ndi thawale limodzilo, ndi ng'ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale;

45. ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomo za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira.

46. Mfumu inaziyenga pa cidikha ca ku Yordano, m'dothe ladongo, pauti pa Sukoti ndi Zaritani.

47. Ndipo Solomo anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinacuruka ndithu; kulemera kwace kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7