Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 6:27-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo anaika akerubiwo m'cipinda ca m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lace la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.

28. Ndipo anawakuta akerubi ndi golidi.

29. Nalemba m'makoma onse akuzinga cipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, m'katimo ndi kumbuyo kwace.

30. Ndipo anakuta ndi golidi pansi pace pa nyumba m'katimo ndi kunja.

31. Ndipo pa khomo la monenera anapanga zitseko za mtengo waazitona, citando ca khomolo cinali limodzi la magawo asanu a khoma lace.

32. Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo waazitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golidi; inde anakutanso ndi golidi akerubi ndi migwalangwayo.

33. Momwemo anapanganso mphuthu zaazitona za pa khomo la Kacisi, citando cace cinali limodzi la magawo anai a khoma;

34. ndi zitseko ziwiri za mitengo yamlombwa pa khomo lina; panali citseko copatukana, ndi pa linzace panali citseko copatukana,

35. Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nakuta zolembazo ndi golidi wopsyapsyala,

36. Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.

37. Maziko ace a nyumba ya Mulungu anaikidwa m'caka cacinai m'mwezi wa Zivi.

38. Ndipo m'caka cakhumi ndi cimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wacisanu ndi citatu anatsiriza nyumba konse konse monga mwa mamangidwe ace onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 6