Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo waazitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golidi; inde anakutanso ndi golidi akerubi ndi migwalangwayo.