Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 4:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Baana mwana wa Husayi ku Aseri ndi ku Aloti;

17. Yehosafati mwana wa Paruwa ku Isakara;

18. Simeyi mwana wa Ela ku Benjamini;

19. Geberi mwana wa Uri ku dziko la Gileadi, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi la Ogi mfumu ya Basani; munalibe kapitao wina m'deramo.

20. Ayuda ndi Aisrayeli anacuruka ngati mcenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.

21. Ndipo Solomo analamulira maiko onse, kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Aigupto; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomo masiku onse a moyo wace.

22. Ndipo zakudya za Solomo zofikira tsiku limodzi zinalr miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,

23. ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.

24. Pakuti analamulira dziko lonse liri tsidya lino la Firate, kuyambira ku Tipsa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya tino la Firate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko,

25. Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wace ndi mkuyu wace, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.

26. Ndipo Solomo anali nazo zipinda za akavalo a magareta ace zikwi makumi anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri.

27. Ndipo akapitao aja anatengetsera cakudya Solomo ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomo, munthu yense m'mwezi mwace, sanalola kanthu kasoweke.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 4