Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 3:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndiponso zimene sunazipempha adakupatsa, ndipo cuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala yina yolingana ndi iwe masiku ako onse.

14. Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzacurukitsa masiku ako.

15. Ndipo Solomo anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la cipangano ca Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ace onse madyerero.

16. Pamenepo analowa kwa mfumu akazi awiri, ndiwo adama, naima pamaso pace.

17. Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo.

18. Ndipo kunacitika kuti tsiku lacitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 3